Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 159
Matigari
Gawo 17
Kumsonkhano womwe Nduna Yoona Zachilungamo inai-
tanitsa kunali fumbi la anthu. Anthuwa anabwera mwaunjinji
chonchi chifukwa anamva zoti ndunayi yabwera kudzathetsa
mavuto omwe anachititsa kuti ogwira ntchito achite sitiraka.
Nayenso bwanankubwa wa m’tauniyo anayendera midzi ingapo
n’kumalimbikitsa anthu kuti akapezeke kumsonkhano womwe
ndunayo inkafuna kuchititsa. Pamsonkhanowu panabweradi
madoda ambiri olemekezeka. Kunabwera oimira maunduna osi-
yanasiyana, achipani cholamula, ogwira ntchito kukhonsolo ya
mizinda yosiyanasiyana, abusa amatchalitchi olekanalekana ko-
manso mabwana oyendetsa fakitale ija. Nawonso ogwira ntchito
kufakitaleyo ndiponso anthu ena okhudzidwa ndi zimene
zinkachitikira ogwira ntchitowo anabwera mwaunjinji.
Dzikoli linali ndi mbiri yabwino kwambiri kumaiko a azungu
chifukwa chowonetsetsa kuti ufulu wa anthu sukuphwanyidwa
komanso kuti mukuchitika ‘chilungamo’ chokhachokha. Chon-
cho, msonkhanowu unakopanso alendo ochokera kumaiko a
azungu omwe anali m’dzikoli. Anthu amenewa anakhala
pamipando yakutsogolo kuti awone bwinobwino mmene mfun-
do za choonadi ndi chilungamo zimatetezera ogwira ntchito!
Nawonso apolisi komanso asilikali omwe anapita kukakhazi-
kitsa mtendere kufakitale ija anabwera kumalowa ndipo anaima
ngati akufuna kumenya nkhondo kunja kwa holoyo. Mkati mwa
holoyo munali apolisi ambirimbiri. Ena anatsamira khoma ndipo
maso awo ankayang’anitsitsa zimene anthu anabwera kum-
sonkhanowo ankachita. Nduna Yoona Zachilungamoyo inavala
suti yakuda yamizere yotuwa. Taye yake yachipani yomwe inali
ndi timizere tofiira komanso tobiriwira inali itamangidwa
pakhosi ndipo inkangoonekera kamfundo kake kokha
158