Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 157

Matigari “Kodi n’zoona kuti dzikoli lasokonekera? Inde ndi zoona. Chimenecho ndi chifukwa chake Mulungu anatumiza mwana wake wobadwa yekha padziko pano kuti adzakonzenso zinthu mogwirizana ndi chikondi chake chosatha. Ukamuuze Guthera kuti, si paja mwati dzina la mtsikanayo ndi limeleli, mukamuuze kuti: Anthu akamadziimba mlandu chifukwa cha machimo ame- ne achita ayenera kudziwa kuti sangapeze mtendere pokhapo- kha atayang’ana pamtanda wa Yesu! Koma wochimwa akalapa n’kusiya machimo ake n’kubwerera kwa ambuye, ambuye ama- mukhululukira chifukwa iye ndi wabwino komanso wokhululu- ka. Usadandaule kwambiri ndi machimo amene wachita usanad- ziwe Ambuye, koma uzidandaula ndi machimo amene wachita utadziwa. Khristu yekha ndi amene angakonze zinthu m’dziko limene lasokonekerali. Iye yekha ndi amene angawongole njira za munthu amene wayamba kuyenda njira yolakwika . . .” “Pa nkhani zandale zija, monga funso lomwe munafunsa lonena kuti mungapeze kuti choonadi ndi chilungamo m’dzikoli, ndikuyankhani mogwirizana ndi mmene Yesu anayankhira Afarisi omwe anapita kukamuyesa pofuna kumuta- pa m’kamwa. Iwo anamufunsa mafunso okhudza ulamuliro wapadzikoli, pomwe ankadziwa bwinobwino kuti ufumu wake unali wakumwamba ndipo likulu lake ndi Yerusalemu watsopano. Yesu anawauza kuti: Perekani za Kaisara kwa Kai- sara, za Mulungu kwa Mulungu. Ndiye nanenso ndikufuna ndikuuzeni kuti: Ngati mukufuna kudziwa za choonadi ko- manso chilungamo chakumwamba, pitani kwa Mulungu wa- kumwamba, yemwe ndi Yesu Khristu amene anapachikidwa pamtanda chifukwa cha inu ndi ine. Koma ngati mukufuna kud- ziwa za choonadi komanso chilungamo chapadziko lapansi, pi- tani kwa anthu amene amalamulira padziko lapansili . . .” 156