Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 155
Matigari
zovala, amene amakolola pamene sanalime uja anatenga zovala
zonse. Nthawi iliyonse yomwe wolima uja wakhetsa thukuta
lake n’kupanga zinthu zooneka zoti zimuthandize, wokolola
pamene sanalime uja ankabwera n’kukokolola zonse. Kenako
wolima uja anapeka nyimbo yosonyeza kusagwirizana ndi
zimene zinkachitikazo:
Sindidzalimanso nthaka kapena kudzala mbewu,
Popeza wokolola pamene sanalime amatenga zonse
Ine n’kumagona kumimba kuli pululu.
Sindidzamanganso nyumba,
Popeza wokolola pamene sanalime amalanda zonse
Ine n’kumagona pamtetete
Sindidzasokanso zovala,
Popeza wokolola pamene sanalime amandilanda
Ine n’kumayenda chinochino
Sindidzapanganso zinthu
Popeza wokolola pamene sanalime ndi amene amalemera nazo
Ine n’kumayenda ndi matumba obooka.
Ine ndakana kukhala ngati poto yemwe amaphika
Yemwe amavutika ndi moto koma osadya nawo!
“Munthu wamkulu ndikuuzeni! Nkhondotu inaulika pakati
pa amene amakolola pamene sanafese ndi amene amalima. Ko-
ma amene amakolola pamene sanalime sanali yekha. Iye limodzi
ndi antchito ake anathamangitsa amene amalima uja mpaka ku-
mapiri, uyo mpaka m’zigwa; anakweranso mapiri, uyo mpaka
m’zigompholera; uyo m’zigwa, m’nkhalango mpaka kuma-
lekezero a dziko. Anthuwa analimbana koopsa. Chaka china-
dutsa. Kenako zaka khumi. Mpakatu zaka miyandamiyanda.
154