Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 154
Matigari
Kodi ndi ndani amene walakwira mnzake, pakati pa Guthera
ndi Mulungu? Kodi ndi ndani amene akufunika kugwada
n’kupempha mnzake kuti amukhululukire? Tandiuzeni, inu
amene mumawerenga malemba: Kodi ndi ndani amene ana-
lenga dziko losokonekerali?”
“Samala m’bale wanga! Samala kuti usachite tchimo lomwe
sungakhululukidwenso!” wansembeyo anatero akuoneka kuti
wazizidwa thupi ndi zimene Matigari ananena. “Kodi ndi chi-
wanda chamtundu wanji chabwera kunyumba kwanga kuno?”
Kenako, atakumbukira kuti wangomaliza kumene
kuwerenga Baibulo. Komanso anakumbukira mphekesera zom-
we zinali ponseponse m’dzikomo, ndipo nkhawa ija in-
amubwereranso. Anayambanso kukayikira. “Kodi amenewa si
mayesero ofanana ndi amene Mulungu anamuyesa nawo Yobu
pamene analola kuti Satana amuyese?”
“Tchimo lake liti?” Matigari anafunsa mopwetekedwa mti-
ma kwambiri.
“Tchimo lonyoza Mulungu! Tchimo lochimwira mzimu
woyera!”
“Ndachimwira mzimu woyera chifukwa ndanena kuti
dzikoli lasokonekera? Talekani ndikuuzeninso ndagi ina yonena
za munthu yemwe amakolola pamene sanalime. ‘Munthu wina
anaswa mphanje, kuphwanya zigulumwa, kuunda mizere, kud-
zala mbewu komanso kumazisamalira. Munthu yemwe
amangokolola asanalime analanda malowo ndipo iyeyo ndi
amene anatenga zokolola zonse. Kenako munthu analima mun-
da uja anamanga nyumba, koma munthu yemwe amakolola
pomwe sanalime uja anabweranso n’kuilanda. Wolima uja ana-
manganso mafakitale abwinoabwino koma munthu amakolola
pomwe sanalime uja anatenga onsewo. Wolima uja anasoka
153