Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 153
Matigari
zija sizinatseguke mozizwitsa. Anadziwanso kuti nkhani zonse
zokhudza mngelo Gabrieli zinali zabodza. Koma anaonabe kuti
munthu ayenera kuonetsetsabe kuti nyali yake ndi yoyaka
nthawi zonse chifukwa zinthu sizidziwika. Kenako anachotsa
chitsokotsoko kukhosi kwake n’kunena kuti:
“Ndagi mwanenayi ndi yovuta kuimasulira. Koma Ambuye
wakumwamba sachita chinthu popanda cholinga. Chilala, njala,
matenda, mavuto, madzi osefukira, zivomerezi, imfa komanso
milili—zimachitika ndi cholinga. Mulungu amachita zinthu m’n-
jira yodabwitsa. Ndipo amaulula cholinga komanso zinsinsi
zake akafuna komanso nthawi yake ikakwana. Ndife ayani kuti
timuuze Mulungu zochita? Mavuto komanso zokhoma zimene
timakumana nazozi ndi ziyeso. Mulungu amafuna kuti aone
kupirira kwathu. Zikanakhala kuti mtsikanayo sanasiye
kupemphera, Mulungu akanamuthandiza kudziwa zoyenera
kuchita. Koma kodi ndine ndani kuti ndiweruze munthu wina?
Komanso kodi ndine ndani kuti ndilande udindo wa Mulungu
n’kumaweruza munthu chifukwa cha zimene wachita? Mwa-
kumbukira nkhani ya mzimayi yemwe anapezeka ndi mwamu-
na wa mwiniwake ija? Kodi Yesu anauza anthu aja chiyani ata-
bweretsa mayi uja kwa iye. Am ene sanayam be wachim wapo at-
ole mwala kuti amugende. Eetu! Ndiye nanenso ndingotsatira mapazi a
Yesu n’kunena kuti: Munthu amene sanayambe wachimwapo at-
ole mwala kuti amugende mtsikanayo. Koma mtsikanayo
ndimuuza kuti: Bwereranso kwa Ambuye, yambiranso
kupemphera kwa Mulungu wako. Ugwade n’kumupempha kuti
akukhululukire . . . ”
Mosazindikira, Matigari anaulula dzina la mtsikanayo.
“Koma kodi ndi tchimo lanji limene Guthera wachita?
152