Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 152
Matigari
yemwe anapangana naye. Mnyamatayo anapita kukatsegula
muselo yomwe munali munthu uja komanso akaidi ena khumi.
Kenako mnyamatayo anakhomanso zitseko zija ndipo anaka-
pereka makiyi aja kwa mtsikana uja, yemwe anakabwezera
makiyiwo m’thumba la wapolisi uja n’kumanamizira kugona.
Wapolisiyo atadzuka, anapeza mtsikanayo akugonabe pambali
pake. Kenako anadzuka mofulumira kuti mabwana ake asamu-
peze akugona muofesi. Mtsikanayo anatuluka n’kumapita. Ko-
ma chisoni chinali chitadzadza mumtima mwake. Iye anali
ataphwanya lamulo la khumi ndi chimodzi lija . . . Ndiye tandi-
uzani, inu amene mumawerenga komanso kutanthauzira
malemba: Kodi ndi pati pamene pali choonadi munkhaniyi? Ko-
di ndi pati pamene pali chilungamo? Kodi n’kuti kumene mun-
thu angakapeze choonadi komanso chilingamo m’dzikoli?
Chifukwatu ndikudziwa ine kuti kumene kuli mtsikanayo ali
ndi chisoni chosaneneka, moti misozi ikungotsika m’masaya
mwake ngati mitsinje. Kodi mundiuza zotani munthu wamulun-
gu? Kodi mundiuza mawu otani omwe angapukute misozi ya
mtsikana ameneyu? Kodi n’chifukwa chiyani Ambuye wa-
kumwamba analenga dzikoli kuti likhale chonchi? Dziko limene
anthu amene amafesa zoipa amakolola zabwino, amene amafesa
zabwino amakolola zoipa! Kodi buku loyera limene mumaw-
erengalo likuti chiyani pa nkhani imeneyi? Tandimasulirani
ndagi imeneyi, ine yankho lake likundivuta. Tandimasulirani
mfundo imeneyi, ine yandikanika kuimasula. Tandiuzeni: Kodi
ndikamuuze chiyani mtsikanayo? Chifukwatu ndinamuuza kuti
ndikakumana naye ndikapeza mayankho a mafunso amenewa . .
. ”
Tsopano wansembeyo anaupezano mtendere mumtima
mwake. Ankangokhala ngati wina wamutula chimwala chomwe
chinali paphewa lake. Iye anazindikira kuti zitseko zandende
151