Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 151
Matigari
akumwamba komanso atate ake apadziko lapansi. Iye
sankalephera kupemphera ndipo sankajomba kutchalitchi. Pa
nthawi ya nkhondo yomenyera ufulu wa dziko lathuli, bambo
ake apadziko lapansi anamangidwa ndi apolisi. Mkulu wa apoli-
si anamuuza kuti bambo akewo akhoza kumasulidwa ngati
mtsikanayo atavomera kugona naye. Mtsikanayo anakana,
ndipo atate ake apadziko lapansiwo ananyongedwa. Iye anatsala
ndi chiudindo chosamalira azichimwene komanso azichemwali
ake. Choncho anapempha atate ake akumwamba kuti:
‘Ndithandizeni kuti ndikwanitse kusamalira abale angawa.’ Iye
anapemphera n’kupemphera. Koma sanapeze chakudya choti
adye, sanapeze zovala zoti avale! Choncho tsiku lina anaganiza
zoyamba kuyendayenda m’tauni. Iye anayamba uhule chifukwa
ankangofuna kupeza ndalama yoti agulire chakudya komanso
zovala. Komabe, kungochokera tsiku limenelo, analumbira kuti:
‘Ambuye, ndithandizeni kuti ndisunge mawu anga. Kuyambira
lero sindidzayerekeza kuchita uhule ndi apolisi omwe anapha
bambo anga komanso ngakhale wapolisi aliyense.
Ndithandizeni chonde, ngakhale kuti ndine munthu wochimwa,
ndipatseni mphamvu kuti ndizitsatira lamulo la khumi ndi
chimodzi limeneli!’ Dzuwa linalowa n’kutuluka, ndipo masiku
anabala zaka. Kenako munthu wina anabwera kuchokera kunk-
halango komwe anthu omenyera ufulu wadziko lino ankabisala.
Munthuyo anapeza apolisi akufuna kulumitsa mtsikanayo galu.
Apolisiwo ankachita zimenezi chifukwa ankamufuna mtsi-
kanayo. Koma mtsikanayo anatsimikiza mtima kuti sangayere-
keze kumayenda ndi apolisiwo. Munthuyo anapulumutsa mtsi-
kanayo. Posakhalitsa, munthuyo anatsekeredwa m’ndende.
Mtsikana uja anapita kwa wapolisi uja n’kukadzipereka kwa iye.
Kenako wapolisiyo anagona tulo tofa nato. Mtsikanayo anaba
makiyi a ndendeyo n’kukawapereka kwa mnyamata wina
150