Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 150
Matigari
“Moti mulibe vuto lina lomwe mungakonde kuti ndiku-
thandizeni . . . mwachitsanzo kusowa zovala, kapena malo ogo-
na?”
“Ludzu komanso njala yanga si ya chakudya kapena cha-
kumwa. Njala komanso ludzu limene ndili nalo ndi lokhudza
nkhawa zanga. Ndazungulira paliponse kufunafuna choonadi
ndi chilungamo.”
“Choonadi ndi chilungamo?”
“Inde.”
“Chatani? Kodi mumapemphera?”
“Ayi. Siine nkhosa yampingo wanu. Koma kungoti mbalame
yotopa imatera pamtengo uliwonse kuti ipume. Ndafufuza
m’misika, m’mashopu, m’mphambano, m’minda, m’makhoti
ngakhalenso m’tchire. Ndayenda ine. Ndakwera m atatu, ngolo,
mabasi, malole, sitima komanso maboti. Ndapitapo kwa apolisi,
oweruza komanso kumaofesi osiyanasiyana a boma. Ndapita
kwa ophunzira pasukulu yaukachenjede ndiponso aphunzitsi,
koma sindinapeze yankho la nkhawa yanga. Kenako munthu
wina anandiuza kuti: ‘Pita kwa munthu wamulungu.’ Ndiye
munthu ameneyo ndi inuyo, si choncho?”
“Inde, mwabweradi kwa munthu woyenerera.”
“Mumawerenga komanso kutanthauzira mawu a Mulungu.
Ndiye ndikufuna ndikutulireni nkhawa yanga yomwe yakhala
ikundisowetsa mtendere kwa nthawi yaitali. Sindikubisirani
kanthu chifukwa sindikukayikira kuti mundipatsa malangizo
enieni ochokera pansi pamtima. Kalekalelo, panali mtsikana
wina. Iye anali wodzisunga pakati pa atsikana a nthanga yake.
Pamoyo wake ankamvera ambuye ake awiri basi: Atate ake
149