Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 15

Matigari Kenako anadutsa apolisi aja n’kumalowera cha kuchikweza china komwe kunali njanji. Maganizo ake anatembenukirano ku njanjiyo, yomwe inalowa pakati pa phiri. Zimenezi zinamukumbutsa zinthu zina moti anakhala ngati wazizidwa. M’maganizo mwake ankadzifunsa kuti, “Ndi miyoyo ya anthu angati yomwe inatayika pamene ankamanga njanjiyi komanso ankaboola phiriri kuti padutse njanji?” Anakumbukiranso bomba lomwe linaphulika pamalowa komanso mfuu za ogwira ntchito omwe anakwiririka amoyo bombalo litagwetsa makoma a phangalo. Anakumbukiranso kubuula koopsa kwa anthu omwe anaphwanyidwa ndi zitsulo zolemera. Zinkangokhala ngati akuona zomwe ankaganizazo. Iye ankakhalanso ngati akumvadi anthu akulira ndi ululu woopsa miyala itawaphwanya komanso ena akubuula mosonyeza kuti akutsirizika. Njanjiyo itangotha kumangidwa, inayamba kumeza masamba atiyi, khofi, thonje, gonje, balele, ndipo tinganene kuti pafupifupi zokolola zonse zomwe zinkakololedwa panthaka yomwe Mtsamunda Williams ndi anzake anaba kwa anthu, zinkatuluka m’dzikoli kudzera panjanjiyi. Bambo uja anaima pamwamba pa phiri n’kuyang’ana kumunsi kwake. Tsopano tauni inali itayala konse mpaka kumunsi kwenikweni kwa phililo. Kumbali zonse kunali mapiri moti ankangokhala ngati mpanda woteteza tauniyo. Bamboyo sanamvetse. Ankati kudzayang’ana kutsogolo kwambiri cha kumapeto a mapiriwo, kenako n’kudzayang’ana tauniyo. Iye anaonadi kuti yakula zedi poyerekezera ndi kale! Apolisi anali ndi galu aja anali akumudutsa tsopano. Iye anawayang’ana mwachidwi pamene ankatsetsereka kulowera nsewu wopita kumunsi kwa tauniyo. 14