Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 149
Matigari
madzi pamene munali ndi ludzu! Anthu amenewa adzalira kuti: Kodi
Ambuye tinakuonani kuti muli ndi njala, muli ndi ludzu, muli osavala,
mukudwala kapena muli kundende kuti tikuthandizeni? Ndipo inu
mudzawayankha kuti: Monga mmene munachitira kwa aang’ono awa
pakati panu, munachitira ine amene—“
Matigari anatsukuluza kukhosi kwake. Wansembe uja
anazindikira kuti mwalowa munthu ndipo anasiya kupemphera
kuja n’kuimirira. Chipumi chake chinkangoti waliwale ngati
malata chifukwa chathukuta lomwe linkatsika pankhope pake.
Mtima wake unkagunda mwamphulupulu, koma anayesetsa
kuukhazika pansi.
“Ndinu ndani?” wansembeyo anafunsa Matigari.
Matigari asanayankhe, wansembe uja anakumbukira
pemphero lake lija komanso zomwe ananena zija, zoti anthu om-
we sanathandize abale ake a Khristu adzaponyedwa ku Gehena
wamoto komwe adzakakukute mano mpaka kalekale. Zimenezi
zinachititsa kuti ayambe kuchita zinthu mwaulemu ndi Matigari,
komabe ankachita zinthu mwamantha.
“Chonde khalansi pansi!” Iye anamulozera Matigari mpando
ndipo anayamba kumulonjera mwaulemu kwambiri.
“Ndikudziwa kuti sindikufunikira kuchita kufunsa, koma
kodi muli ndi njala?”
“Osati kwenikweni.”
“Kapena pali penapake pamene simukumva bwino
m’thupi?”
“Ayi.”
“Kapenatu muli ndi ludzu, si choncho?”
“Ayinso.”
148