Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 148

Matigari Gawo 16 Anapeza wansembe uja atagwada pansi akupemphera. Bai- bulo lotsegula linali patsogolo pake. Anali atavala mkanjo ndipo chapakhosi pake panali kakolala koyera. Zinkaoneka kuti anka- konzekera mwambo wamapemphero. Matigari anangolowa osagogoda m’chipinda munali wansembeyo ndipo anaima pafupi ndi khomo. Wansembeyo sanamuone ndipo anali chogwada kwinaku akupemphera. Nkhani yomwe inkamusokoneza mutu wansembeyo inali yomwe inali paliponse yoti Yesu wabweranso. Iye ankadzifunsa kuti, ‘Nanga bwanji ngati mphekeserazo ndi zoona?’ Choncho iye anaganiza zofunsa Mulungu kuti amuthan- dize kudziwa zenizeni zake za nkhaniyi . . . “ . . . Monga munanenera Ambuye, kuti tiyenera kuonetsetsa kuti nyali zathu zisazime nthawi zonse ngati anamwali asanu ochenjera aja. Popeza anthu awiri adzakhala ali kumunda; wina adzatengedwa pom- we wina adzatsala. Azimayi awiri azidzapera pamphero; wina adzatengedwa pomwe wina adzasiyidwa. Nonse muyenera kukhala okonzeka, chifukwa palibe akudziwa tsiku limene ambuye adzabwere . . . Koma Ambuye pajatu munanenanso kuti popeza palibe amene akudzi- wa nthawi yomwe mudzabwerenso, masana kaya ndi usiku, tsiku ko- manso nthawi, tiyenera kusamala ndi aneneri onyenga. Popeza kud- zabwera aneneri onyenga omwe adzasocheretse anthu okhulupirika, ko- manso kudzabwera a Yesu Khristu onyenga ndiponso aneneri onyenga. N’chifukwatu ndikupempha Ambuye, kuti mutsegule maso komanso makutu anga kuti ndione ndi kukumvani, kaya mubwera kwa ine mukuoneka motani, ndikumvetserani. Chifukwatu paja munanenanso kuti mukadzabweranso, mudzachotsa anthu onse omwe sanabwere kud- zakuonani muli kundende kapena kuchipatala, onse omwe sanaku- patseni chakudya pamene munali ndi njala, kapena kukupatsani 147