Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 147
Matigari
Yovomerezeka komanso akuvina kavinidwe komwe ndi kovo-
merezeka m’dziko. Kungoyambira dzulo, ndalowa m’chipani
cha anthu amantha, moti nanenso ndaphunzira kutseka kamwa
langa kuti lisandilowetse m’mavuto. Mukhoza kunyamuka
tsopano . . . Ayi, tadikirani kaye . . . Ndapeza mfundo inayake . . .
tamvetserani. Ngati mukufunitsitsadi kupeza mayankho a ma-
funso anu, pitani kwa wansembe. Iye sasiyana ndi Baibulo lake.
Iye amangokhalira kuwerenga Baibulo tsiku lonse n’kumalitan-
thauzira kwa anthu. Akhoza kukakuuzani zambiri zokhudza
choonadi ndi chilungamo . . . ”
Matigari anayang’ana mphunzitsiyo. Maso a mphunzitsiyo
ankaonekeratu kuti adzadza ndi mantha. Nkhope yake inali
thukuta lokhalokha.
“Ndikufuna ndikutsineni khutu pang’ono,” anatero Matiga-
ri. “Ndikuchokera kwa wophunzira nyenyezi zamakono. Ndina-
muuza kuti mantha akachuluka m’dziko mumachitika zoipa
zambiri . . . koma si zokhazo. Pali magulu awiri a anthu ophunz-
itsa nyenyezi zamakono: Omwe amakonda choonadi, komanso
ena omwe amachigulitsa.”
146