Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 146

Matigari “Ndiye kuti simundiuza kumene ndingapeze zimenezi?” “Kupeza chiyani? Khatelo?” “Choonadi komanso chilungamo. Pamene tinali kundende kuja, kodi si paja ndinakumvani mukufunsa kuti: ‘Ngati sind- ingaphunzitse choonadi, ndiye ndiziphunzitsa chiyani?’” “Kungochokera pamene tinasiyana dzulo lija, tulo sindina- tione mpang’ono pomwe. Sindinapumenso ngakhale pang’ono. Ndakhala ndikuzungulira m’dzikoli kuti ndipeze munthu ame- ne angandiuze kumene munthu yemwe wadzimanga ndi lamba wamtendere angapeze choonadi ndi chilungamo! Ndinalowa m’tchire ndipo ndinakumana ndi mayi wina yemwe anandiuza kuti: ‘Pita kwa amene amaphunzitsa nzeru zamakono, anthu omwe amaphunzitsa nyenyezi zamakono!’ N’chifukwa chake ndabwera kwanu kuno. Tengani choko chanu kapena cholem- bera chanu mundiuze: Kodi ndi kuti m’dziko muno kumene munthu amene wadzimanga ndi lamba wamtendere angapeze choonadi ndi chilungamo?” “Shiiiiiiiiii! Musamayankhule mokweza kwambiri,” mphunzitsi uja anamuchenjeza Matigari. “Kumbuyo kulibe maso, zimene zachitika dzulo zija tiyeni tiziiwale. Lero ndi tsiku lina. Mawanso lidzakhala losiyana ndi lero. Kodi simunamve kuti aphunzitsi komanso mapulofesa akumamangidwa popanda kuzengedwa mlandu? Tandiyang’anani ineyo. Ndili ndi mkazi komanso ana awiri. Kodi azidzadya chiyani ndikamangidwa n’kukatsekeredwa kundende? Zoona ndimangidwe n’kuzunz- itsa anthu osalakwa chifukwa chokonda kufunsa mafunso basi? Wakuba tinatsekeredwa naye dzulo uja ananena kuti, ‘Munthu wanzeru ndi amene amadziwa kutseka pakamwa pake.’ Ana- wonjezeranso kuti pali anthu ena omwe amapindula m’moyo kokha chifukwa choti akuimba nawo nyimbo yomwe ndi 145