Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 144
Matigari
Ndasiya kufunsa mafunso ambiri. Dokalase ya kuno imatan-
thauza kuchita zimene ukuona kuti zingakuthandize, kuti
ukhutitse mimba yako. Choncho, pano ndiyambe kaye nda-
maliza maphunziro anga, ndidzapeze kaye ntchito kaya ndi ku-
banki kenako ndizidzapeza tindalama toti ndidzagule zinthu
zanga. Kapena ndipeze mwayi woti ndikaphunzire kunja kwa
dziko lino, mwina kupita ku USA . Ndikadzamaliza maphunzi-
ro ndidzabwera kuno n’kutsegula kampani yofufuza zinthu.
Ndidzakhala katswiri wothandiza makampani a ku Ulaya ko-
manso mabungwe ena akunja. Koma ndili ndi funso limodzi:
Kodi ndi kuti kumene munthu angapeze chinthu kapena
kuyambitsa chinthu chomwe chingakhaledi chakechake popan-
da ena kulowelerapo? Ngati muli ndi mafunso ena, mukhoza
kupita kwa akadaulo ophunzitsa nyenyezi zamakono . . . ”
“Kunja kuno kuli ophunzira a mitundu iwiri,” Matigari ana-
ganiza mumtima mwake, “Omwe amakonda choonadi komanso
omwe amagulitsa choonadi. Koma nanga bwanji aphunzitsi
amakono? Aphunzitsi osula anthu kuti adziwe nyenyezi za-
makono?”
Pamene ankachoka, anauza wophunzira uja kuti:
“Mantha aakulu amabweretsanso mavuto aakulu m’dziko.
Munthu akapereka nsembe kwa mzimu wakuba, amangokhala
ngati wauputa kuti ukhale ndi dyera lofuna zambiri kuposa
pamenepo . . . ”
143