Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 142
Matigari
Gawo 14
Wophunzira anali atabindikira kwayekha kwinaku aku-
werenga. Atangomuona Matigari, anayamba kunjenjemera moti
buku lomwe anagwira m’manja mwake linagwera pansi. Sana-
peze mphamvu zouza Matigari kuti akhale pansi.
“Mwabwera kudzatani kuno? Mwabwera kudzatani?”
wophunzirayo anafunsa Matigari akuchita mantha kwambiri.
Matigari anaima kaye phee. Anayamba kuganizira kuti kodi
wophunzira ameneyu ndi yemwe uja amene ndinatsekeredwa
naye limodzi m’ndende? Kodi chamuchitikira n’chiyani kuti
ayambe kuchita mantha chonchi n’kusiya nthabwala komanso
kulimba mtima kwake kuja? Kodi mtima wake wangati wa
mkango uja walowera kuti? Kenako Matigari anayamba ku-
mufotokozera zimene anabwerera.
“Ndayendayenda paliponse m’dziko lino kufunafuna
choonadi ndi chilungamo. Ndinakumana ndi mzimayi m’then-
gomu ndipo anandiuza kuti: ‘N’chifukwa chiyani wasiya
wophunzira nyenyezi zamakono?’ Zimenezo zinandikumbutsa
za iweyo, ndinakumbukira kuti tinamangidwira limdzi muselo
ija dzulo. Ndiyeno ndinadziuza kuti: ‘Inde, si wophunzira uja
anamangidwa chifukwa chofunafuna choonadi?’ Ndinaona kuti
ndiyambirenso kufufuza kwanga. Munthu sayenera kunyozetsa
mphamvu zafumbi limodzi kapena dontho limodzi lamvula.
N’chifukwa chake ndakupeza kuno. Tsegula mabuku omwe
ukuwerengawo ndipo undiuze: Kodi ndi kuti kumene munthu
amene wadzimanga ndi lamba wachilungamo angapeze
choonadi ndi chilungamo m’dziko lino?”
“Tamvetserani,” anatero wophunzira uja, akunjenjemerabe
komanso mantha atamusungunura, “Masiku ano dziko linamera
mano, zinthu zinasintha. Kodi mwamva chilengezo chomwe
141