Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 140
Matigari
ndi chilungamo ndi chintchitodi chachikulu. Koma kaya ndi-
topa chotani, sindisiya kufufuza. Sindingalole kuti ndisiye John
Boy mesenjala, komanso mtsamunda, omwe ali ngati nthata zo-
yamwa magazi, kuti atenge nyumba yomwe ndinavutika kui-
manga ndi manja angawa. Zingatheke bwanji kuti ndimusiye
atenge nyumba yomwe ndinaikhetsera magazi anga? Ndinga-
lolelenji kuti chuma changa chonse chikhale m’manja mwa an-
thu omwe amakolola pamene sanalime komanso mamesenjala
awo achikuda omwe ndi adyera?
Nkhani inanso yomwe inamupatsa mangolomera ndi ya
zimene Guthera komanso Muriuki anachita kuti amupu-
lumutse. Iye anaganizira za Guthera. Kenako anaganizira za
Muriuki. Ululu womwe anthuwa ankamva unasandukano
wake; mavuto omwe ankakumana nawo, anasandukanso ake.
Ankati akakumbukira kuti Guthera anadzipereka ngati
nkhosa yoperekedwa nsembe kuti amupulumutse, ankamva
ululu woopsa mumtima mwake ndipo maso ake ankayamba ku-
yabwa atalengeza misozi. Iye anadzifunsa mobwerezabwereza
kuti: “Kodi ndi kuti, ndi kuti padzikoli komwe choonadi ko-
manso chilungamo chikubisala? Kodi ana anga akhala aku-
zunzika mpaka liti, kusowa pokhala, kuyenda osavala komanso
kugona ndi njala? Nanga kodi ndi ndani amene angapukute
misozi ya azimayi omwe analandidwa malo awo ngati mayi
anakumana naye m’tchire uja?”
Ayi! M’chilengedwemu komanso m’mbiri yonse ya anthu
muyenera muli yankho, Matigari analingalira mozama. Iye
ankafunika kupeza munthu yemwe angamasule mfundo
yomwe yamangidwa pamene pali yankholo, munthu yemwe
angaulule chinsinsi cha m’chilengedwe.
139