Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 14

Matigari Gawo 4 Anayamba kuyenda m’mbali mwa nsewu n’kudutsa Mercedes-Benz ija ndipo nkhani zomwe zinkalengezedwa pawailesi zija zinayamba kumvekera patali. “. . . Dziko la United States lachenjeza dziko la Russia kuti . . . Boma la Soviet Union lauza dziko la USA kuti . . . Dziko la China ndi la India . . . Anthu omwe anapita kumwezi . . . tsopano tifike ku nkhani zamasewero, mpikisano wamagalimoto . . .” Iye anadzifunsa kuti, “N’chifukwa chiyani anthu sakuvala lamba wachilungamo kuti nkhondo komanso zipolowe zisamachitikenso m’dzikoli?” Mu Benz ija munali anthu awiri akuda, mwamuna ndi mkazi, ndipo mwamunayo ankatsopa botolo la mowa wamame, pomwe mkaziyo ankamwa zakumwa zoziziritsa kukhosi. Kenako anasiya kuganizira zomwe anamva kuchokera m’galimoto ija, yomwe tsopano inali itapita. M’ma Benz ena munali azungu okhaokha, ena munali amwenye ndipo ena munali anthu akuda. M’mbuyomo, bamboyu anali dalaivala wa Mtsamunda Williams. Koma pano zinthu zinali zitasinthiratu. Ndi ndani amene akanaganiza kuti tsiku lina anthu akuda angamadzayendetse magalimoto awoawo! Chimene chinali chitatsala tsopano chinali choti azipanga okha magalimoto, sitima zam’madzi, zapamtunda komanso ndege. Kenako anayambanso kuganizira za banja lake. Ankadzifunsa kuti, “Ndiyambira pati kuwasakasaka?” Kenako anatulukira pa ofesi yapolisi yomwe inali m’mbali mwa nsewu uja. Maganizo enanso anamubwerera. “Kodi kapena ndikauze apolisi kuti andithandize kuwasakasaka? Ayi. Ndiwasakasaka ndekha.” Atadutsa polisi ija, anakumana ndi apolisi awiri ali ndi galu wamkulu. Chapafupi ndi pamene anakumana nawopa panali chipatala chaching’ono. 13