Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 139

Matigari kudziwa njira yomwe angadutse m’chipululu komanso m’tchire muno? Anasiyatu kupenda nyenyezi. Pano amapenda Wailesi ya Choonadi . . .” “Ndiyetu pitani kwa anthu omwe amadya mabuku, anthu ophunzira! Nyenyezi zamasiku ano ndi mabuku. Anthu amene amaphunzira zopezeka m’mabuku ndi amene ali anthu anzeru masiku ano. Kodi ukuganiza kuti n’chifukwa chiyani akuzun- zidwa koopsa? N’chifukwa chiyani akukakamizidwa kuti aziim- ba nyimbo ya munthu m’modzi basi? N’chifukwa chiyani akufu- nika kumangobwereza nyimbo imene ikuimbidwa ndi munthu m’modzi yekha, ‘yemwe ndi kalonga wawo?’ Odala ndi anthu amene amazunzika chifukwa choti akufunafuna choonadi, chifukwa maganizo awo ndi mitima yawo imakhala yaufulu, ndipo ndi amene anyamula mfungulo yatsogolo lathu. Koma izi sizikutanthauza kuti onse aona kuwala pa nthawi imodzi, kapena kuti onse amasuka kunsinga za mantha! Tandiuzeni: Ko- di n’zotheka kupeza mwina munthu m’modzi kapena awiri pa- kati pawo yemwe anamasuka ku ukapolo wa mantha kuti ama- sule mfundo ya choonadi n’kuulula zinthu zobisika? Eni, kwa- yaniko chakudya . . . Mukatenga kakhwalala kameneka muk- atulukira mumsewu waukulu . . . Muyende bwino . . . . Ine ndip- itirize kusesa nyansi zomwe zayamba kuunjikana m’dziko mu- no!” Mayi uja anapitirizabe kusesa komanso kuchotsa zinyalala. Matigari anauyambanso ulendo, ndipo mafunso opanda ma- yankho ankangoyendayenda m’mutu mwake. N’chifukwa chi- yani sindinaganize zimenezi poyamba pomwe paja? Kodi wophunzira kusukulu yaukachenjede komanso mphunzitsi uja si anamangidwa chifukwa chofunafuna choonadi? Bwanji ndichite kuyambiranso kufufuzaku. Kufunafuna choonadi 138