Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 138
Matigari
“Mukapitiriza kuchita zimenezi, mapeto ake mufika pamene
ndafika inepa—kumatola zinyalala kwinaku ukuyankhula
wekha ngati wamisala! Anatero mayiyo mokweza kwambiri
ngakhale kuti Matigari anali ataima pafupi naye.
‘Mukuyang’ana chiyani m’tchire muno?’”
“Ndikufufuza choonadi ndi chilungamo,” anatero Matigari.
Mayiyo anaseka, ankaseka mokhala ngati akumumvera chi-
soni komanso pa nthawi imodzimodziyo mokhala ngati
akumunyoza, ndipo kenako anamupatsa madzi akumwa aja.
“M’bale wanga woyendayenda, sungapeze mayankho a ma-
funso ako m’tchire muno, chifukwa simukhala anthu. Choonadi
ndi chilungamo chimapezeka m’zochita za anthu. Cholondola
ndi cholakwika chimaoneka m’zimene anthu amachita. Koma
ngakhale pakati pa anthuwo, ukhoza kuvutika kwambiri kuti
upeze mayankho a mafunso ako. Ukudziwa chifukwa chake? Le-
ka ndichite kukunong’oneza zimenezi, ena angatimvere. Paja
nayonso mitengo ili ndi makutu. Tayandikira. Nd i m antha.
M’dziko muno mwachuluka anthu amantha. Kodi mwambi uja
umati chiyani paja? Mantha akachuluka m’dziko mumachitika
zoipa zambiri. Ndisiyeni ine mumtendere. Nyamukani bambo,
pitani kwa anthu anzeru, kwa anthu omwe amadziwa kupenda
nyenyezi.”
“Kodi anthu amenewo amapezekabe masiku ano?” anafunsa
Matigari. “Inetu ndimaganiza kuti abusa aziweto ndiye anthu
anzeru, chifukwa nthawi zambiri amakhala akupenda nyenyezi.
Nyenyezi zinkawatsogolera akamayenda m’zipululu komanso
m’tchire. Ndi nthawi imene ankayendayendayi yomwe anapeka
nyimbo yodzadza ndi nzeru zochokera kwa nyenyezi. Koma si
amene ndangokumana nawo posachedwapa ataunjikana n’ku-
mamvetsera wailesi, Wailesi ya Choonadi kuti iwathandize
137