Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 137
Matigari
Gawo 12
Iye anayamba kuyang’ana choonadi ndi chilungamo mu
udzu komanso m’tchire. Iye anayang’anayang’ana m’minga, zi-
yangoyango, m’mikwaso, zulu komanso m’zisa za mbalame. Iye
anayang’anayang’ana m’chilengedwe chonse cha m’tchiremo.
Ankangokhala ngati wachita misala. Koma kenako mtima wake
unayamba kugunda kwambiri. Iye anaganiza kuti: “Mlimi sasiya
kufesa mbewu chifukwa choti mbewu ina sinamere. Wofunafu-
na chilungamo satopa mpaka atachipeza. Choonadi sichiwola
kapena kufwifwa. Chilungamo chimaposa mphamvu. Tandiuza-
ni: ‘Kodi n’kuti kumene munthu angapeze choonadi ndi chi-
lungamo m’dzikoli?’”
Kenako atafika m’chigwa china, anakumana ndi abusa a zi-
weto. Atawayandikira, anazindikira kuti abusawo anali ndi
mawailesi awiri. Ina ya Sanyo ndipo ina ya Phillips.
Mawailesiwo anawakweza mogonthetsa mkutu. Onse ana-
watchera pasiteshoni yofanana.
Mwatsegulayi ndi Wailesi Yanu ya Choonadi . . . Pulezidenti
wadziko lino . . .
“Zoona kumvetsera wailesi ntchire ngati muno?” Wailesi ya
Choonadi inali italowa m’malo mwa zitolilo zomwe abusa
amaimba akamafuna kugoneka nkhosa. Kenako anatembenuka
n’kuwasiya abusawo ndipo anayamba kulowera kwina komwe
sankakudziwa. Zimene zinkamveka pamawailesi aja zinkango-
khala ngati zikumupirikitsa kuti achoke m’chigwacho . . .
Kenako anakumana ndi mayi wachikulire akuchotsa
zinyalala panja pakansasa kake komwe kanali m’tchiremo. Tsitsi
la mayiyo linkangooneka ngati chikusa. Zinkaoneka kuti panali
patatha zilimuka chipeso chisanadutsemo. Matigari anapita kwa
mayiyo n’kumupempha madzi akumwa kuti aphe chipemba.
136