Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 136
Matigari
ndi cholakwika? Kodi woipa ndi ndani? Kodi ndi amene
wachititsa kuti munthu wina achite tchimo, kapena amene
wachita tchimoyo? Kodi wolakwa ndi ndani? Kodi ndi amene
wachititsa kuti wina ayambe kuyenda njira yolakwika, kapena
amene wagwidwa akuchita cholakwikacho? Kalekalelo, ana
ankaimba pogwiritsa ntchito zala za m’manja. Ankati:
Chala chaching’ono chinati: Tiye tizipita!
Chala chachiwiri chinati: Kuti?
Mgonapakati anati: Tikabe?
Msonyaalendo anati: Nanga tikakagwidwa?
Mteketeke anati: Ine toto, sindipita nawo.
Kodi n’chiyani chimene chinafunika kukonzedwa
choyamba? Zinthu zimene zikuchititsa kuti munthu achite
tchimo, kapena miyoyo ya anthu omwe akuchita tchimolo?”
“Kodi choonadi ndi chilungamo chabisala kuti pamoyo wa
munthu?”
Iye ankadzimva wosungulumwa. Maganizo oti angochita
zinthu zoti zimuthandize kuti adzipulumutse n’kuiwala
zonse, anamugwira nsukunyu n’kumufoola. Kenako anango-
khala ngati wapenga, moti anasiya kuyenda munsewu muja
n’kulowa m’tchire.
135