Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 135

Matigari Gawo 11 Iye anayenda wapansi. Anakwera ngolo yokokedwa ndi abu- lu komanso njinga. Anayendanso pa m atatu, mabasi komanso malole. Anayendanso pasitima. Iye ankapita kulikonse kumene kukanapezeka anthu. Ndipo m’malo onsewo ankafunsa funso limodzi: Ndi kuti kumene munthu yemwe wadzimanga ndi lam- ba wamtendere angapeze Choonadi ndi Chilungamo? Ndiye popeza m’mitu mwa anthuwo munali mukungoy- endayenda mphekesera yomwe inali ponseponse m’dzikolo, iwo ankangomuyang’ana Matigari posamvetsa kuti akuwafunsa chi- yani. Nkhani imene ankafuna kumvetsera inali yonena za Yesu, Gabrieli, Matigari ma Njiruungi, nkhani yonena za kutseguka kodabwitsa kwa ndende, kuthawa kwa akaidi ndi zinga zangati zimenezi . . . Tsikulo linali longoti zii. Silinali lotentha komanso silinali lo- zizira. Kunalibe dzuwa, komanso kunalibe mvula. Nyengo inali chapakatikati. Nkhawa inali itamumanga manja ndipo zinkaoneka kuti palibe akumusamala. Linali goli lolemera la mafunso opanda mayankho, omwe anali nawo koma palibe akanamuyankha. Chomwe chinkamuchititsa mantha n’choti anali yekha amene anali ndi khawa yowoletsa mafupa ngati imeneyo m’dziko lon- selo. Zinkangokhala ngati ali yekheyekha pakati pamadzi. Koma nkhani imene inkamusowetsa mtendere kwambiri inali yokhudza Guthera. Ankati akakumbukira mmene anamupu- lumutsira, mafunso ambirimbiri ankaswana m’mutu mwake. “Zikanakhala kuti . . . zikanakhala kuti . . . komaa!” Iye ankadzi- funsa kuti: “Kodi choonadi chimathera pati, nanga bodza lima- yambira pati? Kodi n’chiyani chimasiyanitsa chabwino ndi choipa? Kodi pali kusiyana kotani pakati pa choyenera 134