Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 133
Matigari
Ophunzira awiri apasukulu yaukachenjede anamangidwa dzulo
atapezeka ndi mabuku oletsedwa m'dziko muno . . .
Ophunzira enanso anamangidwa atagwidwa akuchita ziwonetsero
zosonyeza kusagwirizana ndi zimene boma la United States komanso
mayiko ena a ku Ulaya akuchita pothandiza boma la ulamuliro
watsankho la ku South Africa. Ophunzira amenewa agamulidwa kuti
akakhale kundende zaka zisanu. Pamene ophunzirawa amatengedwa
n'kumapita kujere anayamba kukuwa kuti: Chipambano ndi chathu!
Wophunzira yemwe amafuna kuyambitsa chipani chake wauzidwa
kuti asiye kulitokosola dala boma . . . M'dziko muno muli chipani
chimodzi chokha basi. N'chifukwa chiyani ophunzirawa akufuna
chipani china? Mtsogoleri wa dziko lino, Pulezidenti Ole, wanena kuti
ophunzira amenewa ayenera kukhala okhutira ndi chipani chimodzi
chimene chili mādziko muno, chomwe ndi chipani cholamula.
Nduna Yoona Zachilungamo yayambapo ulendo wake woyendera
midzi ya m'dziko muno. Zikunekanso kuti ikachezera kampani ya An-
glo-American Leather and Plastic Factory. Ikapita kumeneku ikakambi-
rana ndi oyendetsa kampaniyi komanso ogwira ntchito. Pafakitaleyi
panachitika chipwirikiti dzulo pamene apolisi amalimbana ndi ogwira
ntchito omwe amachita ziwonetsero. Ogwira ntchito omwe anakwiya
ndi kuchepa kwa malipiro anawotcha ziboliboli za oyendetsa kampani-
yi. Malipoti akusonyeza kuti apolisi akanapanda kulowererapo, ndiye
kuti ogwira ntchitowo akanaimbidwa mlandu woopsa woononga ko-
manso kuwotcha zinthu mwadala. Zimenezi zikanachitika ndiye kuti
chuma cha dziko lino chikanakhudzidwa kwambiri.
Chidziwitso chapadera . . . chidziwitso chapadera . . . Mneneri wa
boma wanena kuti anthu asamamvetsere zomwe ena akunena zoti
mngelo Gabrieli watulutsa akaidi mndende ina komanso kuti mkaidi
m'modzi anali Yesu Khristu. Iye anati zimene anthu akufalitsazi zoti
Yesu kapena Gabrieli wabweranso ndi bodza lankunkhuniza. Boma
132