Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 131
Matigari
Matigari anatulukira, ndipo anapeza munthu akuyankhula
n'kumaloza kumene iye anatulukirako akunena kuti, "Chokani
kagwereni uko!"
Kenako anawapatsa moni:
"Tandiuzeni abale anga! Kodi ndi kuti m'dziko muno ku-
mene munthu angapeze choonadi ndi chilungamo?"
"Mwati chiyani?"
"Ndikufunafuna choonadi ndi chilungamo m'dziko muno!"
"Zokuonerani mungabwere kuno kukhoti kuti mudzafune-
fune choonadi ndi chilungamo?"
"Koma mmesa kuno n'kumene kumapezeka oweruza ko-
manso maloya?" Matigari anafunsa.
"Kodi mukufuna ndiyankhe funso lanuli mosabisa mawu?"
"Inde. Ndikufuna chilungamo chenicheni chomwe chazikid-
wa pa choonadi."
"Ndikupatseni kaye malangizo. Pitani mukapeze chingwe
cholimba bwino, kenako mukadzimangirire. Inutu moyo
simukuufuna, apo ayi mutu wanu sukuyenda bwinobwino . . .
Akakumverani mukufunsa mafunso amenewa akupititsani ku-
manda kuti mukadikirire . . . "
Matigari ananyamuka n'kumapita akusowa chonena.
130