Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 130

Matigari "Iwe ukuganiza bwanji? Tangoganizani, kodi ndi kuti ku- mene kuli tchalitchi chakale kwambiri padziko lonse? Ku Ethio- pia, ku Africa. Kodi Yesu ali mwana anathawira kuti limodzi ndi makolo ake? Ku Egypt, ku Africa. Zomwe zinachitika kalekalelo zikhozanso kuchitika masiku ano. Ngati ataonekera kwa ine, ndikhoza kumugwira dzanja, kumugwadira n'ku- muuza kuti: ‘Ambuye, tithandizeni anthu ooneka ngati osanun- kha kanthufe kuti tikhale patsogolo.’ Kenako ndingakhale kud- zanja lake lamanja n'kumuuza kuti: ‘Taonani azungu komanso nthata zachikudazi. Taonani, a Boy komanso a Williams akubwera kwa inu. Chonde apirikitseni pamaso panu n'ku- waponyera kumoto wosatha komwe munakonzera anthu opondereza anzawo komanso ankhanza. Chifukwatu inu mu- nali wanjala, koma sanakupatseni chakudya; munali ndi ludzu, koma sanakupatseni madzi; munkayenda osavala, koma sanakupatseni chovala. Munkadwala, koma sanabwere kud- zakuonani. Komanso pamene munali kundende, sanabwere kudzakuzondani. Ambuye, musamvetsere mapemphero awo! Kodi mwamva mafunso awo achinyengowo? Iwo akufunsa kuti: Ambuye, kodi tinakuonani kuti muli ndi njala, muli ndi ludzu, muli wosavala, mukudwala komanso muli kundende kuti tikuthandizeni? Mudzawauze choonadi Ambuye. Mudzawaonetse apo pagona chilungamo chanu! Mudzawayankhe kuti: ‘Ndikukuuzani kuti, monga mmene mu- nachitira kwa aang'ono awa ali kundende, munachitira ine amene.’ Mudzawathamangitse Ambuye. Mudzawauze kuti, ‘Tiyeni uko anthu ochimwa inu! Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo komanso oipa inu, omwe muli okonzeka kugulitsa dziko komanso abale anu! Chokani kagwereni uko!’” 129