Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 13

Matigari ndi atsamunda aja? Ndiye zatani kuti ayambe kuchita zimenezi poyerayera?” . . . Mukumverayi ndi Wailesi Yanu ya Choonadi. Nduna Yoona Zachilungamo yanena kuti dziko lathuli ndi la anthu ogwira ntchito. Ndipo yachenjeza ogwira ntchito onse kuti asiyiretu kugwirizana ndi anthu omwe akumasokoneza mtendere m’makampani ponena kuti akufuna awonjezeredwe malipiro. Antchito omwe akumachita zimenezi sakusiyana ndi asilikali omwe amasokoneza mtendere komanso kumafuna kulanda boma . . . Boma lalamula kuti m’dziko muno musapezekenso chipani chotsutsa . . . Mtsogoleri wa dziko lino, Pulezidenti Ole, wanena kuti bomali ndi la anthu . . . ndipo anthu m’dziko muno sakufuna kuti mukhale zipani zotsutsa chifukwa zimabweretsa chisokonezo. 12