Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 129

Matigari "Kungoti nyuzipepalayi sinanene zinthu zambiri. Anthu akumanena kuti kunamveka mabingu komanso kunachita ziphaliwali pa nthawi imene zimenezi zimachitika! Aliyense amaganiza kuti kugwa mvula, koma sikunagwe dontho ngakha- le limodzi. Ndipo mosadziwika bwino, mabingu komanso ziphaliwali zija zinasiya." "Ndi ndani akudziwa, mwina ndi ziphaliwalizo zomwe zi- natsegula zitseko zandendeyo? Komansotu akuti chitsekocho anachipeza mmene chinalili chosathyoka kapena kupindika paliponse. Komanso makoma anali mmene analili." "Zimenezitu ndi zodabwitsa kwambiri. N'chifukwa chiyani anthu ena amanena kuti zozizwitsa sizichitika? Amafuna ataona chiyani kwenikweni?" "Mukudziwa, anthu ena akamaliza kuwerenga zozizwitsa zonse zomwe Mose anachita amaganiza kuti zimenezo zango- khala nthano chabe za m'Baibulo." "Zoona, zozizwitsa zimachitikadi. Tsiku lina ndinaona mun- thu akutulutsa nkhunda m'chisoti chake komanso akutulutsa ndalama zapepala za ma 5 Shillings kuchokera mumphuno mwa mwana wazaka zitatu." "Basi siyani nkhani zabodzazo! Mmene ichepera mphuno ya mwana wazaka zitatumo n’kutuluka 5 Shillings? Zafodya basi! Chinthu chimene ndikulakalaka nditadziwa n'choti, kodi Matig- ari ndi ndani kwenikweni?" "Kodi simunamve zoti Baibulo limanena kuti adzabweranso kachiwiri?" "Kodi mukutanthauza kuti ndi uja aneneri ananena kuti adzabweranso? Mwana wa Munthu?" 128