Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 128

Matigari Gawo 8 Kenako ananyamuka n'kupita kumabwalo amilandu. Anthu onse omwe ankaimbidwa milandu patsikulo ankangoganizira za Matigari. "Bwanji naye Matigari osabwera kuno n'kudzandimasura munsinga za maunyolowa kuti ine ndikhale mfulu?" "Kodi ukuganiza kuti angakwanitsedi kukuchitira zimene- zo?" "Kodi simunawerenge?" "Anthu olemba manyuzipepala sagona, amagona kapena? Kodi adziwa bwanji zinthu zomwe zachitika dzulo usiku, ndikunenatu dzulodzuloli?" "Amanyuzipepala anena kuti sikuti zinachitika usiku kwam- biri. Kupolisiko kunali wapolisi m'modzi basi ndipo ena anali atapita kufakitale kukamenya komanso kukalondera ogwira ntchito omwe amapanga ziwonetsero aja. Wapolisi m'modzi yekha ndi amene anatsala ndipo amaphika ugali. Nyuzipepa- layo inati, wapolisiyo analumbira kuti anaonetsetsa kuti watseka zitseko zonse za selo yomwe anatsekera akaidiwo, kuzimitsa magetsi, kenako n'kuika makiyiwo m'thumba n'kupita kukakha- la padesiki yake. Koma kenako atabwerera kuselo kuja, anakapeza kuti kulibe aliyense. Loko anali adakali pachitseko. Palibe paliponse pamene panathyoledwa kapena kupindika mwa njira iliyonse. Wapolisiyo ataona zimenezi anangogwera pansi n'kuyamba kupemphera kwa Mulungu wakumwamba: 'Mundikhululukire Ambuye pakuti ndine munthu wochimwa! Ndikupempha kuti mundiuze ngati lili dzanja lanu limene lawa- tulutsa, monga mmene munachitira kalelo ndi Paulo ku Ndende ya ku Kaperenao!'" 127