Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 127

Matigari Kenako anaona munthu ataima pafupi ndi tiyi. "Tandiuzeni abale anga! Kodi ndi kuti kumene munthu an- gapeze choonadi komanso chilungamo m'dziko muno?" "Kodi ndi ndaninso akufunsa mafunso oduka mutuwo?" "Ndinu ndani achikulire?" "Ndine wofunafuna choonadi ndi chilungamo," Matigari anayankha. "Ingobwererani kumene mwachokerako mukakumane ndi munthu wina dzina lake Matigari ma Njiruungi. Ameneyo ndi munthu amene akudziwa bwino tanthauzo la nyimbo mukuimbayo ya 'choonadi ndi chilungamo.' Mukakumana naye mumufunse kuti: Popeza chilungamo n'choposa mphamvu, ko- di mphamvu za chilungamocho zimachokera kuti?" 126