Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 126
Matigari
“Zimenezo ndi zimene Matigari ma Njiruungi amanena:
‘Azungu nonse komanso atchito anu onse, ukooo! Dzikoli lili
ndi eni ake.’”
“Koma ndiye anawauza chilungamotu!”
“Zoonadi.”
“Inde zoona, choonadi chenicheni.”
“Ine ndakhala ndikunena kuti: Kodi anthu osakonda dziko
lawowa adzapita kuti anthu omenyera ufulu wadziko lathu
akadzabwerera, akubangula ngati mikango n'kumanena kuti:
‘Ife okonda dziko lathu tabwera! Nonse ogulitsa dziko lathu
chokani!’”
“Kodi ndi zoona kuti zinthu zidzasinthiratu? Koma ngati
zinthu zitapitirira mmene zililimu bola kukayembekezera ku-
manda ndithu. Zoona anthu obwera, kaya ndi a ku Ulaya
kapena ku Amerika, azipeza malo omanga mahema awo, ma-
hema oti asungiremo zida zankhondo, mahema oti azisungira-
mo zinthu zomwe atibera, ife eni ake anthu akuda tikusowa
pokhala? Komanso mabwana achikuda kwinaku atatanganidwa
kusokoneza maganizo a anthu ndi lilime lokha uchi komanso
pogwiritsa ntchito apolisi kuti azitseka anthu pakamwa
powazunza?”
“Nawenso wanena zofanana ndi mfundo zoluma ndi
choonadi zomwe Matigari ananena. Matigari ndi wosagonjet-
seka chifukwa atangomumanga anawauza kuti: ‘Musasangalale
chifukwa choti mwandiponyera kudzenje lamdima. Mundionan-
so ndikutulukira pakangotha masiku atatu.’”
“Tatiuzeni nthuni! N'chifukwa chiyani Matigari ma Njiruun-
gi sanabwere kuminda kuno? Akanabwera ndikanamuuza kuti:
Musabwerere m'mbuyo . . .”
125