Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 125
Matigari
atangofika pagetiyo mahatchiwo anangoima chii. Iwo anaye-
setsa kuwamenya kuti aziyenda, koma mahatchiwo sana-
wamvere mpang’ono pomwe chifukwa cha mantha.”
"Zimangokhala ngati zimene inachita hatchi yomwe inaona
mngelo wa Ambuye ataima pamsewu ija?"
"Sinalitu hatchi, anali bulu!"
"Mukanganabe tikamaliza, pano tikufuna timve kaye nkhani
ya Matigari!"
"Kenako anamuona ataima pakati pamsewu, mkono wake
umodzi uli m'chiunomu. Winawo atanyamula lupanga loyaka
moto."
"Mwamva zimene wanenazo! Lupanga loyaka moto!"
"Kenako anawauza kuti: 'Ndinu nthata zoyamwa ena maga-
zi! Ndibwezereni makiyi a nyumba yanga komanso mundibwe-
zere malo omwe munalanda abale anga!'"
"Tabwerezanso! Mwati ananena kuti chiyani? Anati azungu
onse komanso nthata zachikuda zichite chiyani?"
"Anati abweze chuma chomwe anaba kwa eni ake!"
"Zimenezotu ndi zoona. Anawachita bwino anthu osayamika
amenewa omwe amangokhalira kutipondereza. Anthu amenewa
akhala akutikama mkaka kwa nthawi yaitali. Dzulo anali
azungu obwera limodzi ndi antchito awo. Leronso ndi omwewo
akutizunza, kungoti avala nkhope zina. Kulikonse ungalowere,
kaya ndi kumafamu, kaya kumafakitale, ukawapeza ali phathi-
phathi, bwana ndi wantchito wake. Kodi anthu omwe timavuti-
ka kugwira ntchitofe tidzamera liti mnofu wabakha, tidzamwa
liti tiyi wamkaka?"
124