Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 123

Matigari “Amenewa ndi malaulo ndithu! Ndi ndani amene analotapo kuti m’dziko mwathu muno anthu angamadzayankhule mopan- da mantha choncho? Ndi ndani akanaganiza kuti tsiku lina an- thu angadzasiye kuyenda nyominyomi chifukwa cha mantha? Kuti nthawi ingadzafike anthu n’kusiya kumachita mantha kuyankhula zinthu zomwe zikukhudza miyoyo yawo?” “Ayi, tiyeni tingodekha mwina tsiku limenelo lingadzafike! Dzulodzuloli tinalawako mmene zidzakhalire titamuona Matig- ari akuchita zinthu ngati mkango. Galu komanso apolisiwo anachita mantha zedi n’kuchoka.” “Koma mmesa apolisiwo anali ndi mfuti?” “Ngakhale zikanakhala kuti iweyo unali ndi mfuti, nawenso ukanangosowapo mofanana ndi mmene apolisiwo anachitira. Mawu ake okha anali ngati chiphaliwali ndipo maso ake aman- goti lawilawi ngati moto! Utsi wankwiyo wake umatulukira m’makutumu, pakamwa komanso mumphuno.” “Koma Matigari ndi patali! Ndikanakonda ndikanakhalako kuti ndimugwire chanza komanso kumuimbira nyimbo yomwe anthu a ku Tram pville anapeka ija yakuti: Ndionetseni munthu Yemwe dzina lake ndi Matigari ma Njiruungi, Yemwe akamayenda m’mapazi mwake m’malira maberu. Komanso zipolopolo, ngindee! Komanso zipolopolo, ngindee! “Ukutanthauza kuti bwenzi ukuimba utamukumbatira mwachikondi?” wina anafunsa mochenjera. Atangonena izi pakamwa pa azimayiwo panaphwethuka ndi chimwemwe, moti anayamba kuseka chikhakhade kwinaku aku- thethetsa m’manja mwathabwa. 122