Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 122
Matigari
“Mantha. Mantha akachuluka m’dziko zotsatira zake zima-
khala mavuto osaneneka.”
”Mawuwa ndi amene Matigari anawauzanso anthuwo.”
“Munthu wochepa thupi komanso wamfupi n’kulimba mti-
ma choncho? Mwamunadi ndi mumtimamu, kokha mchepera
wa kalulu!”
“Kodi mwanena kuti ndi wamfupi? Inetu ndamva zoti ndi
chiphanza, munthu wamphamvu zake. Ndi wamtali zedi moti
akhoza kugwira mitambo!”
“Mwati bwanji?”
“Inde, ndi wamtali ngati nsungwi moti mutu wake umagun-
da kumwamba!”
“Musandiuze atsikana! Kenako chinachitika n’chiyani?”
“Kodi n’chiyaninso chimene ndingakuuzeni amwali chomwe
simunamve? Kenako, atayamba kuyenda, imvi zake komanso
makwinya omwe anali pamphumi pake zinabalalika. Chithunz-
ithunzi chake chinayamba kutalika n’kumalowera cha uko.
‘Tamusiyani mtsikanayo msanga! N’chifukwa chiyani mukuzun-
za mayi wadziko lino!’ Anawauza choncho apolisiwo.
‘Tangoyerekezani kutambasula dzanja lanu n’kumukhudza
muone!’”
“Oh, musandiyendetse thupi mache, zoona anthu omenyera
ufulu wadziko lathu lino adakalipo! Koma samachita mantha?”
“Kuchita mantha n’chiyani? M’mabukutu mwa anthu ome-
nyera ufulu mulibe mawu akuti ‘mantha.’ Simungakhulupirire
nditakuuzani kuti anabwerezanso kuwachenjeza apolisiwo kuti:
‘Tangoyerekezani kumukhudza mtsikanayo muone! Mudziwa
kuti mukusewera ndi munthu wotani. Mundidziwa ine Matigari
ma Njiruungi!’”
121