Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 121

Matigari Gawo 6 Kenako anapita pankhumano ya nsewu wina. Azimayi om- we ankachokera kumtsinje kukatunga madzi, anatula mitsuko komanso zidebe zawo n’kuyamba kukambirana za Matigari. “Ndi mfupidoli komanso wochepa thupi, amangooneka nga- ti ndi munthu wamba basi.” “Ndi wokalamba?” “Akuonekadi kuti ndi wachikulire ndithu. Koma sikuti ndi nkhalamba yogwa n’kumina.” “Kani nayenso ndi wathupi losayamikira chakudya?” “Ingodekhani kuti ndikuyalireni kaye nkhani yonse! Nkhani ndi kamnyamata amwali. Zikumveka kuti gulu la anthu apamsi- ka linaima n’kumangoonerera wapolisi akuzunza mtsikana winawake pomuopseza ndi galu.” “Koma kodi apolisiwa apitirizabe kutionerera chonchi mpa- ka liti? Kodi kale lija, azungu asanabwere n’kuyamba kutila- mulira, kunali apolisi komanso asilikali? Ayi ndithu! Tinali ndi ndende m’dziko muno? Ayi! Kodi kunkachitika zinthu zophwanya malamulo ngati mmene zilili masiku ano? Ayi ntheradi! Zinthu zinkayenda bwino pamene tinkadzilamulira to- kha. Ndikunama kapena?” “Izizi tikambabe, tiyeni timve kaye nkhani ya Matigari.” “Mtsikanayo amalira koopsa kwinaku akunjenjemera. Koma anthu omwe anaunjikana pamalowo anangoima ngati zikwang- wani n’kumangoonerera. Zimangokhala ngati matupi awo apan- gidwa ndi mantha. Mwinanso tinene kuti zimangokhala ngati m’mitsempha yawo mumayenda mantha m’malo mwa magazi.” 120