Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 120

Matigari ya Matigari? Akutisokoneza bwanji!” “Kodi ndinu ndani akulu? Ndinu Bambo Wofunafuna Choonadi ndi Chilungamo?” “Mwalasa ndithu, ndinedi,” Matigari anayankha. “Anzanufetu tikukambirana nkhani yochititsa chidwi. Kapena yakudutsanitu! Koma ndiyambe ndakulumani khutu kaye. Ngati mukufuna kupeza choonadi komanso chilungamo, choonadi chenicheni chosathira mchere, pitani kwa mneneri amene wabwera m’dziko lathuli, yemwe mbiri yake yagwedeza dziko teketeke.” “Dzina lake ndi ndani? Nanga ndingakamupeze kuti?” “Dzina lake ndi Matigari ma Njeruungi. Ngaruro wa Kiriro amamudziwa. Iye amanena kuti wakumana naye dzulodzuloli.” 119