Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 12

Matigari Mumtima mwake ankati, “Munthu akamayenda ulendo wapadzikoli amakumanadi ndi misampha komanso mayesero ambiri.” Analowa m’munda wina n’kudutsa pakati pa zikanga za mitengo ya maluwa ndipo kenako anatulukira mumsewu waphula. Anaima kaye n’kudzayang’ana kumanja, kenako kumanzere. M’mbali mwa nsewuwo munali magalimoto akuda a mtundu wa Mercedez-Benz omwe anali ndi mikolamawu. Kenako anamva mawu kuchokera m’galimoto yomwe inali kutsogolo kwake. Inali wailesi ndipo inkati: . . . Mwatsegulayi ndi Wailesi Yanu ya Choonadi . . . Mtsogoleri wadziko lino, wolemekezeka Pulezidenti Ole, wanena kuti pasapezeke anthu akuyenda m’magulu a anthu oposa asanu. Iye sanafotokoze zambiri zomwe zachititsa kuti alamule zimenezi. Koma zikuoneka kuti ana a kuyunivesite akonza zopanga ziwonetsero panja pa maofesi a akazembe a dziko la Britain ndi America posonyeza kusagwirizana ndi zomwe mayikowa akuchita popitirizabe kupereka zida zankhondo komanso ndalama ku ulamuliro watsankho wa dziko la South Africa . . . Mtsogoleri wathu Pulezidenti Ole wanena kuti akuyamikira kwambiri asilikali a dziko la Britain omwe mwezi watha analanda zida asilikali omwe amafuna kulanda boma. Anati mnzako weniweni amaoneka pakagwa tsoka. Pulezidenti Ole, wayamikira kwambiri zimene dziko la Britain linachita polola kuti asilikali ake ena atsale m’dziko muno kuti aphunzitse asilikali athu kumenya nkhondo. Pamsonkhano wina, Pulezidenti Ole anabwerezanso zimene ananena pa nthawi yomwe asilikali a dziko lino ananyanyala ntchito. Iye anati: “N’zomvetsa chisoni kuti asilikali a boma ananyanyala ntchito kuti awonjezeredwe malipiro titangolandira kumene ufulu wathu wodzilamulira. Bwanji sankachita zimenezi pamene tinkalamuliridwa 11