Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 119

Matigari Ndi la ife ogwira ntchito komanso alimi!’ Mawu amenewo ali m’kamwa, ogwira ntchitowo anayamba zilope n’kubutsa moto ziboliboli za Robert Williams ndi John Boy! Mphepo ya chipo- lowechi inawafika apolisi moti posakhalitsa anatulukira ali limodzi ndi asilikali. Ogwira ntchitowo atangoti maso thaa pa apolisi ndi asilikaliwo, onse anayamba kuthawa. Koma mwatsoka pamene amatuluka n’kuti njira yonse itatsekedwa. Apotu ndiye anakhala ngati awaika pampani. Onse anali pakati pa apolisi ndipo kumbuyo kwawo kunali mpanda wafakitale moti analibiretu kothawira. Popeza kunanjatidwa anthu mi- yandamiyanda, anangoganiza kuti asandutse fakitaleyo kukhala jere.” “Ndiye Ngaruro wa Kiriro ananena zotani zokhudza Matiga- ri ma Njiruungi? Tatitambasulirani bwinobwino. Kodi anatenga uthenga wotani kuchokera kwa Matigari ma Njiruungi?” “Kodi ndi uthenga wotaninso umene mukufuna? Iye anati mapindu onse ayenera kupita kwa amene amagwira ntchito mwakhama.” “Zimenetu Matigari ananena ndiye choonadi ndi chilunga- mo chenicheni. Zoona mlimi azigwira ntchito n’cholinga chokhutitsa anthu omwe amangokolola pamene sanalime? Dzu- lo anali azungu. Lero azunguwo angochita chipiriganyo ndi an- thu akuda.” Matigari analowa m’chipinda chogulitsira zakudyacho n’ku- khala pansi. Kenako anaitanitsa kapu yake ya ntenthandevu. “Abale anga tandiuzeni, kodi ndi kuti m’dziko muno ku- mene munthu angapeze choonadi ndi chilungamo?” Atangonena zimenezi, anthuwo anatembenuka n’ku- muyang’ana. Ankadzifunsa kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi wotani? Sangaone kuti tikukambirana nkhani yosangalatsa 118