Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 118
Matigari
Gawo 5
Iye anapita m’malo ogulitsira zakudya. Anthu ankachita
chidwi kwambiri ndi nkhani ya Matigari moti ena anaiwaliratu
kumwa ntenthandevu wawo komanso kudya chakudya chawo.
Iwo anangokhala n’kumamvetsera, makutu ali petupetu
m’mwamba.
“Ndi Ngaruro wa Kiriro amene anayamba kumuzindikira.”
“Ngaruro wa Kiriro? Ndakhalatu ndikunena ine kuti Nga-
ruro wa Kiriro ndi wozindikira komanso amaona patali.”
“Mwana uja ali ndi nzeru zachibadwa.”
“Koma kumenekooo! Patsogolo ndi ndani? Patsogolo ndi
Ngaruro wa Kiriro!”
“Kodi mukudziwa zimene zimachitika pamene Ngaruro wa
Kiriro amayankhula pamsonkhanowo? Mitima ya anthu onse
imanyamuka m’malele moti zimangokhala ngati aliyense wad-
zozedwa usilikali. Aliyense anali wokonzeka kunyamula zida
n’kuyamba kulimbana ndi anthu oponderezawa. Mawu ake
anali otsitsimula komanso olimbikitsa zedi moti ngakhale mun-
thu akanakhalira mbaula yoyaka moto sakanazindikira kuti
akupsa. Iye anati: ‘Tayani kutali mantha anu chifukwa sitili to-
kha! Abale athu omenyera ufulu wadziko lathu abweranso.’
Zimenezo ndi zimene anawauza. Anawafotokozeranso mwatsa-
tanetsatane zimene zinachitika kuti akumane ndi Matigari ko-
manso mmene Matigari amayankhulira m’mafanizo komanso
m’miyambi kuti: ‘Phindu liyenera kubwerera kwa ife anthu om-
we timakhetsa thukuta m’dziko muno.’ Iye ananenanso kuti an-
thu opondereza anzawo komanso amene amawayang’anira
ayenera kupakila nsanza zawo n’kuona msanawanjira. Ngaruro
wa Kiriro anawafunsa kuti: Kodi eni ake a dzikoli ndi ndani? Og-
wira ntchito onse anayankhira limodzi kuti: ‘Ndi ifeeee!
117