Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 116
Matigari
‘Lolani ana adze kwa ine.’ Koma anawo anachita mantha kwam-
biri moti anangotembenuka n’kulangiza mapazi. Ndi mwana
m’modzi yekha amene anamutsatira.”
“Ndikuuzeni anthuni, si bwino kumanyoza munthu kapena
kumuchitira chipongwe kokha chifukwa cha mmene wavalira
komanso mmene akuonekera. Sizidalira kuti munthu akhale
chiphanza kuti akhale mpulumutsi. Ndikanasangalala kwambiri
ndikanakumana naye pamasompamaso. Ndikanakonda n’kana-
muona pompano kuti ndimugwire chanza . . . ”
Ndiyeno Matigari anatulukira pafupi ndi gulu la anthulo
n’kuima pakhonde.
“Abale anga tandiuzeni chonde. Kodi ndi kuti m’dziko muno
kumene munthu angapeze choonadi komanso chilungamo?”
Anthuwo anangoti chetee n’kumangomuyang’ana ndi diso la
nkhwezule. Ankamuyang’ana monyodola kwambiri ngati
mmene munthu angayang’anire wamisala yemwe akuvina
mosagwirizana ndi nyimbo imene yafika pakolasi n’ku-
masokoneza anzake. Kenako anayamba kuyankhulana n’ku-
madandaula kuti munthuyo akuwaonongera nyimbo yawo
yomwe inali itafika pa tiso we.
“Kodi munthu ameneyu akunenanso chiyani?”
“Nayenso ndi wopanda nzeru bwanji, zoona angatisokoneze
tikukambirana nkhani yofunikayi pomafunsa mafunso opanda
mchere?”
“Bwanji akuleka kungopita ku Wailesi ya Choonadi kuti aka-
funse?”
“Akhoza kupita kwa Nduna Yoona Zachilungamo ngati aku-
funa kumva zambiri.”
115