Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 115
Matigari
Gawo 4
Matigari anapita m’malo ogulitsira malonda. Anazungulira
ponseponse pomwe akanapeza anthu. Anapita kwa ogulitsa
m’magolosale komanso kwa ogula malonda omwe ankadzadza
m’mashopu komanso m’makonde ake akukambirana nkhani . . .
“Ana ndi amene anali oyambirira kumuona.”
“Ana? Ndiye kuti anawauza anawo kuti iyeyo ndi Matigari?
Pajatu mwana ndi mfumu sasiyana zochita, amagwirizana
kwambiri. Komatu paja ana ndi ana basi, amaluma bere lomwe
likuwayamwitsa!”
“Bwanji? Anachitanso chiyani?”
“Eti anayamba kumugenda. Anamubongetsa nayo miyala.”
“Kumugenda? Koma amadziwa kuti munthu akumu-
gendayo ndi ndani?”
“Ayi.”
“Koma nawonso ana amasiku ano! Bwanji osachita manyazi
kugenda munthu wamkulu! Nanga akanamuchotsa diso?”
“Pamenepo ndi pamene pali podabwitsa. Mwalatu ngakhale
umodzi sunamukhudze.”
“Musakhaletu mukuchulukitsa nkhaniyi ndi malovu! Mwati
bwanji?”
“Miyalayo imati ikamamuyandikira, imangosanduka nkhun-
da n’kuuluka.”
“Nkhunda?”
“Inde! Mukuganiza kuti zimenezi zingangochitika?”
“Anawo anayamba kuchita mantha. Kenako kunabwera an-
thu ena n’kuyamba kuwafunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani muku-
genda munthu wachikulileyu?’ Koma Matigari anati:
114