Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 114

Matigari “Inde! Akuti akufuna zinthu zonse zomwe anazikhetsera thukuta. Nawonso akufuna kudya thukuta lawo!” “Mwati bwanji? Tabwerezaninso.” “Anthu okonda dziko lawo aja adakalipooo!” “Kodi mwamuona munthuyo, kapena mwangomva?” Aliyense ankafunitsitsa kudziwa yankho la funso limeneli. Kodi Matigari anali ndani? Kodi amaoneka bwanji? Pa nthawi imeneyi, Matigari anafika pamene panali anthu paja. Anaima chapafupi n’kuwapatsa moni. Onse anatembenuka n’kumuyang’ana. “Abale anga, kodi mungandiuze kumene munthu angapeze choonadi ndi chilungamo m’dzikoli?” Onse anamuyang’ana modabwa. Ena ankang’ung’udza mwamwano. Kenako anatembenukanso n’kuyamba kupitiriza nkhani ankakambirana zija. “Kodi munthu ameneyu akufunsanso chiyani? Ife tikufuna timve kaye nkhani zokhudza Matigari ma Njiruungi! Kodi anza- thu munamuonako? Amaoneka bwanji? Ndi chiphona eti?” 113