Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 113

Matigari Gawo 2 Tsikulo kunalibe dzuwa. Kunalibenso mvula. Kunja sikunka- tentha komanso sikunkazizira. Linali tsiku lotopetsa. Gawo 3 Matigari anapita m’misika yambirimbiri kukasakasaka choonadi komanso chilungamo. Anthu ankakhala m’magu- lumagulu kukambirana nkhani yomwe inadya moto m’dzikolo. “Nkhani yake iti?” “Simunamve?” “Zotani?” “Nkhani yodabwitsa yangochitika kumeneyi?” “Mukuganiza kuti ndingaime pano n’kumakufunsani chin- yezi kubafa? Mukuganiza kuti ndikanaima pano ndikanakhala kuti ndaimva?” “Anthu omwe anathawira kunkhalango ajatu abweranso?” “Anthu ake ati?” “Kodi zoona mukufuna tichite kukuuzani chilichonse? Kodi simungaganize nokha kuti a Matigari ma Njiruungi ndi ndani? Kodi ntchito ya ubongo wanuwo ndi chiyani? Mukufuna udzingowolerana m’mutumo?” “Zimenezotu ndi nkhambakamwa chabe! Mukuganiza kuti anthu amene aja adakalipo?” “Ndi zimenetu tikukuuzanizi! Mphekesera zikunena kuti anthu aja abweranso atanyamula malupanga oyaka moto m’manja mwawo!” “Malupanga oyaka moto?” 112