Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 112

Matigari ankawafotokozera mwatsatanetsatane. Nkhaniyi inapereka chochita kwa anthu ambiri ndipo ochuluka ankasangalala kwambiri akamakambirana nkhaniyi. Iwo ankati: “Koma nkhaniyi ndiye ndi yochititsa chidwi bwanji! Zingatheke bwanji kuti zitseko zandende zitseguke zokha? Kodi Matigari ma Njiruungi ndi ndani?” Anthu a m’mudzi mwa Trampville anapeka nyimbo yonena za Matigari ma Njiruungi. Nyim- boyo inkati: Ndionetseni munthu Yemwe dzina lake ndi Matigari ma Njiruungi, Yemwe akamayenda m’mapazi mwake m’malira maberu. Komanso zipolopolo, ngindee! Komanso zipolopolo, ngindee! 111