Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 111

Matigari Maboma a USA komanso la Soviet Union apita patsogolo kwambiri pa nkhani yotumiza anthu kupulaneti la Mars komanso mapulaneti ena. Malipoti amene atipeza anena kuti . . . Tsopano tibwere ku nkhani zomwe zachitika kwathu konkuno. Mal- ipoti akusonyeza kuti dzulo apolisi anabalalitsa ogwira ntchito pa- kampani ya Anglo-American Leather and Plastic Works ndipo zibolibo- li za akuluakulu ena oyendetsa fakitaleyi, zomwe zinali panja pafakitaleyo, zatenthedwa ndi moto. Zibolibolizi zinali za Robert Wil- liams ndi John Boy. Apolisi anaphulitsa utsi wokhetsa misozi kuti aba- lalitse ogwira ntchitowo. Ogwira ntchito ena amangidwa. Nduna Yoona za Chilungamo ikachezera fakitaleyi kuti ikathetse kusamvanaku. Ino ndi Wailesi yanu ya Choonadi. Malipoti ena omwe angotipeza kumene kuchokera kwa apolisi anena kuti wapolisi wina anakomoka atazindikira kuti akaidi omwe anawatsekera muselo athawa. Choda- bwitsa kwambiri n’choti loko yemwe anakhomera selo yomwe ana- watsekerayo anali nga pachitsekocho. Nazonso zitsulo zotchingira chip- indacho zinali mmene zinalili zosapindika paliponse. Wapolisiyo anali adakali ndi mulu wamakiyi otsegulira zitseko za ndendeyo m’nthumba mwake. Apolisi akufufuzabe kuti adziwe kuti anthuwo athawa bwanji. Tsopano tifike ku nkhani zamasewera. Mumva nkhani zokhudza mpikisano wamahatchi, galimoto, gofu komanso mpikisano wothaman- ga . . . “Basi tatsekani wailesiyo! Ee, koma zimenezi ndiye ndi zoda- bwitsatu!” anatero ana aja ndipo pamalowo panangoti wowowo. “Muriuki, tatiuze! Kodi Matigari ma Njiruungi ndi ndani kwenikweni?” Anawo anamwaza nkhaniyo ngati fumbi. Iwo ankapita kwa anthu onse omwe anali ndi ludzu lomva nkhaniyi ndipo 110