Matigari
Matigari ma Njiruungi.
Mwatsegulayi ndi Wailesi Yanu ya Choonadi . . . Mtsogoleri wa
dziko lino Pulezidenti Ole analandira ndalama zokwana 50 Shillings
kuchokera kwa anthu ena abizinezi dzulo. (Akuda ndi azungu omwe).
Anthuwo anapita kukakumana naye kunyumba kwake. Ndalama imene
anaperekayo ndi yoti ipite kuthumba la apulezidenti lothandiza ana
olumala. Mtsogoleri wa amalondawo anayamikira Pulezidenti Ole
pothetsa chisokonezo chomwe asilikali anayambitsa ponyanyala ntchito
ati chifukwa izi zikanachititsa kuti m’dziko muno musakhale bata ndi
mtendere . . .
Aphunzitsi ena a sukulu yaukachenjede anakaonekera kukhoti dzu-
lo chifukwa chopezeka ndi mabuku a Karl Marx komanso V. Lenin om-
we anasindikizidwa ku China. Mabuku onsewa ndi onena za ufulu wa
ogwira ntchito, ndipo makamaka omwe anasindikizidwa ku China ndi
oletsedwa m’dziko muno kungochokera pamene tinalandira ufulu
wodzilamulira . . .
Ophunzira asanu a kusukulu yaukachenjede amangidwa dzulo
popanga nawo ziwonetsero panja pa maofesi a kazembe wa ku Britain
komanso United States. Ophunzirawa anachita ziwonetserozi posonye-
za kusagwirizana ndi zimene mayikowa akuchita pothandiza boma
latsankho la ku South Africa. Zimene anachitazi ndi zoletsedwa chifu-
kwa pulezidenti wa dziko lino ananena kuti pasapezeke munthu wochi-
ta ziwonetsero m’dziko muno.
Lipoti lina lochokera ku Johannesburg, South Africa, lanena kuti
anthu ena omenyera ufulu wawo achipani cha ANC ndi amene akugan-
iziridwa kuti anaika bomba muhotela ina yomwe azungu amakonda
kupitako. Azungu a m’dzikoli anena kuti akuchita mantha kwambiri
ndi zigawenga za SWAPO komanso ANC . . .
109