Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 11

Matigari Kenako anayasamula ngati akufuna kumeza munthu. Sizinali zochita kufunsa kuti anali atatheratu. Chifukwa cha kutentha, iye ankadzifunsa kuti, “N’chifukwa chiyani dzuwali likutentha chonchi m’mawa uno ngati wina walituma?” Posakhalitsa anayamba kuwodzera. Koma maganizo aja anamubwereranso. Ankadzifunsa kuti, “Ndibwerera bwanji kunyumba ndekhandekha? Zitheka bwanji kuti ndipite kunyumba ndili ndekha? Kodi si paja pakhomo pamafunika kukhala mwamuna, mkazi komanso ana? Tsonotu ndidzuke kuti ndipite m’milagamu ndikawauze anthu kuti tagonjetsa adani athu. Ndikasonkhanitse anthu anga, achibale, akazi komanso ana anga. Tonse tikasonkhane pamodzi n’kubwerera kunyumba yathu. Kali konkha n’kanyama nthuni. Kodi n’kuiwalilanji kanyimbo kankakoma kuimba tili ana kaja? Chikondi ndichoo, Pakati pa akazi ndi ana. Timagawana ngakhale nyemba imodzi Yomwe yagwa pansi panthaka. Kenako anadzuka n’kuvala chisoti chake chija, kunyamula chijasi chake ndipo anachiponyanso paphunzi n’kulunjika kumene maganizo ake anapotokera. Iye ankafunitsitsa akanapita kaye kukaona nyumba yake, koma maganizowa akamubwerera, ankadziletsa n’kupitirizabe kuyenda molunjika m’tauni. Iye anali atatsimikiza mtima. Ankafuna kuti apite kaye kukafunafuna anthu ake choyamba. Ankafuna kudziwa kumene anthuwo akukhala, zomwe amadya ndi kumwa komanso zomwe amavala. Komabe, mtima wake unkamuthawathawa. Ankafunitsitsa akanapita kukaona kunyumba kwake, koma ankaonanso kuti sangapiteko yekha. 10