Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 107
Matigari
Kenako anamva munthu akutsegula zitseko zomwe zinali
m’njira yolowera kuseloyo ndi makiyi kuti kolokochokolokocho.
Ankadzifunsa kuti: ‘N’chifukwa chiyani wapolisi akuyenda mo-
zemba choncho mumdima, osayatsa magetsi?’ Onse anachita
mantha aakulu. Kenako anamva kutsegula pakhomo laselo lawo
lija. Pa nthawiyi aliyense anali ndi mantha ndipo anakonzeka
kuti akumana ndi zoopsa. Kenako anamva mawu chapansipan-
si.
“Tulukani nonse. Osapanga phokoso komanso osayang’ana
m’mbuyo! Mukafika mumsewu, iwe Matigari, ukadikire pafupi
ndi chipatala chija. Enanu mukapitirize kuyenda osayang’ana
m’mbuyo!”
Onse anatuluka mwakachetechete ndipo chifukwa cha mdi-
ma anafufuza khomo n’kutuluka. Makomo onse anali otsegula
ndipo pamalo ofikira alendo panalibepo munthu aliyense.
Ankangokhala ngati akulota!
Ena ankangoganiza kuti akuona masomphenya. Iwo
anatulutsidwa m’ndendeyo ndi munthu yemwe sanamuone.
Ndiye pamene ankayenda n’kumalowera chakumsewu, ambiri
ankadzifunsa kuti: ‘Kodi Matigari ma Njiruungi, munthu wotha
kutsegula zitseko za ndende, ndi ndani kwenikweni?’
Kungochokera tsiku limenelo, mbiri ya Matigari inabuka
ngati moto ndipo inafalikira m’dziko lonse. Iye anakhala
mpulumutsi. Anthu anayamba kumugomera. Koma ambiri
ankadzifunsabe kuti: ‘Kodi Matigari ma Njiruungi ndi ndani?’
106