Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 106
Matigari
kudzachitika chiphwando chokonzekera kubwereranso
kunyumba kwathu!”
“Kodi mukuganiza kuti mutuluka mwachangu kuno?” anag-
widwa akungoyendayenda m’tauni uja anafunsa. “Kubwera
kundende kuno ndi kophweka. Koma kuti utuluke pamakhala
matatalazi. Ndikukhulupirira kuti mukhalabe muli kuno pofika
mawa, mwinanso mpaka tsiku mukunenalo.”
“Ndikanakhala kuti sindinayambane ndi bwana komanso
wantchito wake, zikanakhalako bwino,” wogwira ntchito uja
anatero. Ndazindikira kuti bwana ndi wantchito amenewa san-
gasiyane ndipo akhala akutizunza kuyambira kale. Aliyense
amadziwa kuti Robert Williams ndi John Boy amangokhala nga-
ti ana amapasa omwe anabadwa mimba imodzi n’kuyamwa
bere lofanana. Komanso mukudziwa? Apolisi onse m’dziko mu-
no ali m’manja mwa anthu amenewa. Ngakhalenso makhoti.
Choncho ndikuganiza kuti ungakhale mwayi waukulu ngati
mungatuluke mwachangu kuno. Ndithu mvula yamatalala ikho-
za kugwa tsiku limenelo. Mungokonzekeretsa maganizo anu
kuti muwolera kundende konkuno. Monga mmene mwambi
wina uja umanenera, ndende inamangidwira amuna.”
“Ngakhalenso azimayi!” wina anawonjezera motero.
“Komanso ana.”
“Ndi mngelo Gabrieli yekha amene angakutulutseni kuno.
Ame!” wamowa uja anatero.
Asanamalize kunena mawu amenewa, anamva mtswatswa
komanso phokoso lamakiyi mumdima. Mofulumira anazimitsa
makandulo aja ndipo onse anakhala chete ataunjikana malo
amodzi.
105