Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 105
Matigari
“Kodi ukunena kuti ndine kazitape?” munthu uja anauza
wokupha munthu uja.
“Kodi munamva zoti akazitape amavala zikwangwani pachi-
pumi pawo zolembedwa kuti: ‘Onani, ndine kazitape!’” waku-
pha munthu uja anayankha.
“Aliyense pano akhoza kukhala kazitape wa apolisi.”
Zinkangokhala ngati akufuna kubayana ndi mipeni ndipo
mipeni yawoyo inkawala ndi kandulo yemwe anali muselolo.
“Tasiyani pansi mipeni yanuyo!” Matigari anawalamula ndi
mawu amphamvu. “N’chifukwa chiyani mukusolola mipeni
kuti mubayane? Kodi mavuto mwapalamulawa sakukukwanira-
ni?”
Kenako anthu aja anasunga mipeni yawo ija. Ndiyeno mwa-
na wasukulu uja anati: “Komatu tilipo anthu asanu ndi m’modzi
okha muno. Ndiye sipangakhale kazitape pakati pathu, Yudasi
palibe.”
Matigari anapitiriza kuyankhula ngati kuti palibe chimene
chinachitika.
“Mukufuna mudziwe zimene ndikufuna kuchita? Ndikuuza-
ni, chifukwa ine sindibisa mawu. Ndabwera kuno nditadziman-
ga ndi lamba wamtendere. Mlimi yemwe zomera zake siziku-
tuluka samatopa ndi kubzala. Munthu amene akufunafuna chi-
lungamo samatopa mpaka atachipeza. Choonadi sichimaola.
Choncho choonadi chidzalamulira pangatalike. Ngati si lero
ndiye kuti ndi mawa. Nyumba yanga ndi yanga basi. Sikuti
ndikufuna kuba ya mwini wake ayi. Ndikungofuna zinthu zom-
we ndinamanga ndi manja anga. Mawa ndi tsiku langa. Ndiku-
kuitanani nonse kuti mubwere kunyumba kwanga mkucha,
ndikunena mawa ndiye tsiku linalo. Mubwere chifukwa
104