Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 104

Matigari kumatchena; wogwira ntchito ayenera kudya phindu la ntchito yake!’” “Zimene mwanenazo ndi zoona,” mlimi uja anatero. “Kodi alimife tizidya movutikira chifukwa chiyani? Kodi womanga azi- gona panja chifukwa chiyani? Nanga telala azivala nsanza chifu- kwa ninji?” “Ndiye mutanino?” ena aja anapitiriza kumufunsa Matigari. “Ngati Boy ndi Williams sakupatsani nyumba yanu mutani?” “Tandimvetserani,” anapha munthu uja anauza Matigari. “Kodi wina wanena chiyani posachedwapa? Munthu wanzeru ndi amene amadziwa kutseka pakamwa pake. Ndikufuna ndikubwerezereninso mawu amenewa chifukwa munthu amene samvetsera zonena za anzake sangakhale mtsogoleri. Nkhalango yomwe ili mumtima mwa munthu simayera. Munthu amayenera kusankha bwino mitengo yoti adule mumtima mwake komanso yoti aisiye. Tonse tangokumana kuno. Ine sindikukudziwani, in- unso simukundidziwa. M’dziko muno mwachuluka akazitape. Amatuta nkhani zomwe amva n’kukazikhuthura kwa apolisi. Paliponse pamene mwapeza anthu khumi ndi awiri ata- sonkhana, m’modzi wa iwo ndi Yudasi, ndi kazitape. Ndikukuu- zani ine kuti: Ngati dzina lanu linatamulidwa pankhumano wa ogwira ntchito uja lero, apolisi ayenera ayamba kale ku- kufunafunani.” “Apolisitu akufunafuna chimunthu chooneka ngati chipho- na,” mwana wasukulu uja anatero, akuoneka kuti ali ndi phwete. Koma anayesetsa kudzigwira kuti asaseke. Kenako wokupha munthu uja komanso munthu ankafunsa mafunso uja anatulutsa mipeni yawo kamodzim’kamodzi. Zimenezi zinachi- tika n’kuthwanima kwa diso. 103